Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports Sports

Osewera wakale wa Silver Strikers wamwalira

Osewera wakale watimu ya Silver Strikers Mike Robert, wamwalira kamba kavuto la impso kuchipatala cha Kamuzu Central munzinda wa Lilongwe.

Mng’ono wake wa Mike, Jacob,yemwe amasewera mutimu ya Blue Eagles, wati mkulu wakeyu wakhala akuvutika ndi nthenda ya impso kwa nthawi yayitali.

Jacob wati Mike pakatipa anadwalanso malungo aakulu amene anathamangira ku ubongo ndipo lero chamma 4 koloko kumadzuloku ndi pamene wamwalira.

Jacob watiuza kuti padakali pano dongosolo la mwambo wa maliro silinadziwike.

Mike anakhalako mtsogoleri wa osewera atimu ya Silver ndipo amachokera m’boma la Dowa.

 

Olemba : Praise Majawa

Related posts

MP urges churches to combat rising suicide cases

Rabson Kondowe

Zomba Chingale legislator sent out for violating rules of the House

Romeo Umali

Kuchedwa kwa nsewu wa Ilomba kwadandaulitsa boma

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.