Apolisi ku Limbe munzinda wa Blantyre amanga Rodrick Kaliwo wazaka 28 pomuganizira kuti wakhala akubera anthu powanamiza kuti amachulukitsa ndalama m’matsenga.
Kaliwo anamangidwaponso pamulandu ngati womwewu.
Ofalitsankhani wapolisi ku Limbe, Aubrey Singanyama, wati Kaliwo anatenga ndalama yokwana K60,000 kwa munthu wina wa bizinesi pomunamiza kuti adzayichulukitsa kukwana K900,000 mmaola awiri okha.
Zitakanika, mkuluyu anauza munthu wabizinesiyo kuti akatenge dothi la mtumbira wa manda omwe angokwiliridwa kumene, zomwe zinamudabwitsa kenako anakanena kupolisi.
Apolisi atafika kunyumba kwa Kaliwo, anapeza zinthu zosiyanasiyana zomwe amanamizira anthu kuti iyeyo ndi sing’anga.