Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Oganiziridwa za “Bakili Muluzi TV” akudikira kumva za belo

Bwalo la milandu la Magistrate munzinda wa Lilongwe likuyembekezeka kupereka chigamulo pa pempho la belo la a  Chiyanjano Mbedza, amene akuwaganizira kuti amafalitsa nkhani zabodza patsamba la mchezo  limene amalitcha  Bakili Muluzi TV.

Loya wawo, Gilbert Khonyongwa, ndiye anapereka pempholi  lachitatu sabata ino.

Mulanduwu umayembekezeka kuyamba nthawi ya 9 koloko mmawa uno koma wachedwerapo kaamba koti akudikira oweruza.

Mbedza anamangidwa pa 22 July chaka chino mu mzinda wa Blantyre.

 

Olemba ndi ojambula: Emmanuel Chikonso ndi Thokozani Jumpha

Related posts

Pasuwa backs international newbies at Flames

Romeo Umali

REGION 5 GAMES PREPS IMPRESS COUNCIL

MBC Online

Communication is key for development — NBM

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.