Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

NYA isankha Chakwera

Chipani cha National Youth Alliance (NYA) chati mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) yemwenso ndi mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazaurus Chakwera ndi yekhayo ali ndi kuthekera koyendetsa dziko lino kaamba ka masomphenya ake.

Mtsogeleri wa chipanichi, a Vasco Madhlopa, ndi amene anena izi munzinda wa Mzuzu pa msonkhano wa atolankhani.

Iwo analangiza aMalawi kuti asayike pampando anthu omwe ayenera kupuma pa ndale komanso omwe anawononga chuma cha dziko komanso chisankho cha m’chaka cha 2019.

A Madhlopa ati dziko la Malawi likufunika atsogoleri omwe angathe kulitukula, mmalo moyika pa utsogoleri anthu adyera.

Poyankhulapo pa za migwirizano imene yakhala ikuyambika koma kumathera panjira, iwo ati izi zikuchitika kaamba ka vuto ladyera ndipo anati zaonekeratu kuti migwirizano yotere ilibe tsogolo.

Olemba: Grant Mhango

Related posts

Kalembera wa chisankho cha makhansala sanaime, atero a MEC

Alinafe Mlamba

Zinthu zambiri zasintha — Chithyola Banda

Romeo Umali

Thupi la Dr Chilima aliyika m’manda

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.