Sukulu ya ukachenjede ya Emmanuel imene ndi ya mu mnzinda wa Lilongwe yalengeza zoyamba kuphunzitsa Kiswahili ngati phunziro lapadera.
Izi zadziwika pa mwambo okondwelera chilankhulochi kumene kuli kazembe wa dziko lino mayi Agnes Kayola amene akuyembekeza mtsogoleri wa dziko la Tanzania mayi Samia Suluhu Hassan kuti achite zoyankhula kudzera pa uthenga wa pa kanema.
Pa malo amene pakuchitikira mwambowu pakuyankhulidwa ziyankhulo za Kiswahili, Chichewa ndi Chingerezi.