Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News

Ntchito yokonza msewu kwa Msakambewa yayambanso

Anthu okhala mdera la mfumu yayikulu Msakambewa m’boma la Dowa ayamikira boma kamba kobweretsa kontalakita wina kuti akonze msewu wa Dzaleka-Ntchisi -Malomo, umene akuti wakhala nthawi yayitali osakonzedwa.

Kontalakita oyamba anayamba ntchitoyi m’chaka cha 2022 ndipo pakadali pano, kontalakita wa kampani ya CR20 ndiyemwe akhale akumanga msewuwo, umene ndiwa makilomita 67.

Yemwe anaimira mfumu yayikulu Msakambewa, a Siniyo Gulupu Thotho ndiwo anathokoza pamwambo opereka ntchitoyi m’manja mwa kontalakita watsopanoyu.

Iwo ati kuyambanso kumangidwa kwa msewu wa Dzaleka-Ntchisi-Malomo kuthandiza alimi a mderali kumakukagulitsa mbewu zawo mosavuta kumadera ena.

Khansala wa kuzambwe kwa dera la Msakambewa, Eliza Chulu, wati ndiokondwa ndi kuyambaso kumangidwa kwa msewuwu chifukwa anthu ambiri akhala ndi mwayi opeza ntchito.

A Chikondi Chisale, amene anaimira nduna yazaulimi a Sam Kawale, yemwenso ndi phungu waderali, ati boma ndilodzipereka poonetsetsa kuti anthu akhale ndi msewu wabwino. Iwo alangiza anthu mderali kuti apewe nchitidwe wakuba katundu pomwe ntchito yomanga msewuwu yayamba, ponena kuti izi zimabwezeretsa chitukuko m’buyo.

Ntchito yomanga msewuwu igwiridwa kwa zaka zitatu ndipo itenga ndalama zokwana K92.8 billion.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Karonga District Council cracks whip on uncomplying mill operators

MBC Online

President Chakwera to respond SONA questions

Timothy Kateta

Prison promotes reintegration of ex-cons

Rudovicko Nyirenda
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.