Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Nkhalango zikupitilira kusakazidwa

Unduna owona za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo wati ndiokhumudwa ndimomwe anthu akupitilizira kuononga nkhalango m’dziko muno.

Mmodzi wa akuluakulu ku undunawu, a Titus Zulu, ndiwo ayankhula izi ku Lusangazi m’chigawo chakumpoto pamene amapereka zipangizo zotetezera nkhalango kwa anthu amene amakhala m’midzi yozungulira nkhalango ya Viphya.

A Zulu ati ndizomvetsa chisoni kuti nkhalango zikupitilira kutha, zomwe zikuonjezera mavuto a kusintha kwanyengo m’dziko muno.

“Kuononga nkhalango ndikudzipweteka tokha chifukwa munkhalangoyi mumapezeka zinthu zambiri zotithandiza ife tomwe ngati anthu,” anatero a Zulu.

A Steven Kalanga a ku Lusangazi kulandira zipangizo

Iwo anati kuononga nkhalango kukupangitsa kuti mvula isamabwere mokhulupirika komanso kuti mitsinje idziphwa, zomwe anati zikusokoneza chikonzero cholimbikitsa ulimi wamthilira.

A Zulu anati poona kuti antchito oteteza nkhalango akuchepa, unduna wawo waganiza zogwilira ntchito yoteteza nkhalangozi ndi anthu okhala mozungulira nkhalangozi.

Wolemba: Henry Haukeya

Related posts

Dr Chakwera apereka ulemu omaliza kwa malemu Dr Chilima ku Nyumba ya Malamulo

Rabson Kondowe

Prezidenti Chakwera akhala nawo pa mwambo operekeza maliro

Mayeso Chikhadzula

Lero tapereka holo-yi ndipo pompano tiyamba kumanga chipatala – Troughton

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.