Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Local Local News Nkhani

‘Mtayakhasu ndi ulimi othana ndi njala’

Alimi achitsanzo amene ali mu ndondomeko yokhala ndi chakudya chokwanira pakhomo alangiza alimi anzawo m’dziko muno kuti ayike chidwi paulimi wa mtayakhasu.

Iwowa ali mu nthambi yachitukuko ya mpingo wa Salvation Army imene ikugwira ntchito kwa mfumu yayikulu Mwanza m’ boma la Salima.

M’modzi wa alimi a chitsanzowa, a m’mudzi wa Chikhawo kuderali, a Matsaka Machira, ati ulimiwu ndi othandiza chifukwa amatha kukolola chimanga chambiri pamalo ochepa.

Iwo ati pa ulimi wachaka chino, akolola matumba 11 olemera ma kilogramme 50 limodzi pa munda wa mamita 39 mu litali ndi mamita 16.2 mulifupi, zomwe ati zithandize kuthana ndi vuto la njala chaka chino.

Mlangizi wa ndondomeko yolimbitsa ntchito zaunkhondo, kukhala ndi chakudya chokwanira pabanja komanso kupilira ku mpingowu, a Blessings Mwalwanda, anati ndi cholinga chawo kubweretsa njira zamakono za ulimi pothana ndi njala kaamba ka kusintha kwanyengo.

Pakadali pano, a Lloyd Tiopanyasi a m’mudzi wa Kachigulu, mfumu yayikulu Khombedza m’boma la Salima, apempha mpingowu kuti ufikirenso m’mudzi mwawo chifukwa ati njirayi ndi gwero la phindu paulimi m’dziko muno.

 

Related posts

Balaka robbery suspects in custody

Romeo Umali

All set for 2024 National Youth Summit – NYCOM

Romeo Umali

Bullets open Airtel Top 8 with a victory

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.