Mnyamata wochokera dera lamfumu yaikulu Mwanza m’boma la Salima, Chinsinsi Luka, yemwe ndi alubino, tsopano wati ndiwosangalala kamba kanyumba yomwe boma lamumangira.
Nyumbayi ndimbali imodzi ya ntchito yomanga nyumba kwa anthu achi alubino yomwe mtsogoleri wadziko lino anaikhazikitsa.
Unduna wa zamalo komanso unduna owona kuti pasamakhale kusiyana pakati pamayi ndi abambo apereka nyumbayi kwanyamatayu ndi banja lake lero.
Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, a Jean Sendeza, alimbikitsa anthu m’dziko muno kuteteza anthu achi alubino.
Ndipo nduna ya zamalo, a Deus Gumba, ayamikira ntchito yamtunduwu, kunena kuti ndichitsimikizo kuti boma limaganizira umoyo wa aliyense m’dziko muno.
Pakali pano, boma lamanga nyumba za anthu achi alubino m’dziko muno zokwana 65.