Kampani ya Paramount Concrete Products yati sikutekeseka ndi mmene yayambira masewero season ino timu FCB Nyasa Big Bullets mu ligi ya TNM.
Mkulu wa kampani yi, a Arthur Kalinde, anena izi lero munzinda wa Blantyre potsatira kugonja kwa timuyi dzulo ndi Silver Strikers pa bwalo la Kamuzu.
Bullets yapambana masewero atatu, kufananitsa mphamvu kasanu ndi kugonja kamodzi ndipo yatolera ma pointi 14. Iyo ikusiyana ma pointi 11 ndi timu ya Silver.
Koma a Kalinde ati izi zisafooketse ochemelera chifukwa iyi ndiyo nthawi yoyenera kupereka chilimbikitso kwa osewera.
Paramount Concrete Products imapereka ndalama zokwana K75,000 kwa osewera yemwe wachita bwino kuposa onse, timu yi ikapambana kapena kufananitsa mphamvu.