Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

M’nyamata wa zaka 17 adziombera chifukwa cha chikondi

M’nyamata wazaka 17 zakubadwa, Tinasha Mtawali, wafa atadziombera ndi mfuti ya mtundu wa pistol ku Chitipi munzinda wa Lilongwe chifukwa anasemphana chichewa ndi bwenzi lake, malinga ndi ofalitsankhani ku Polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu.

Iwo ati Mtawali anachoka kwawo ndikupita malo ena osadziwika kumene anayimbira lamya bwenzi lakelo ndi kumuuza kuti sadzamuonanso ndipo ali mkati mokambirana, adamva phokoso la kuwomba kwa mfuti kenako sanamvekenso.

Zitatero, a Chigalu ati bwenzi la malemuwa linakanena za nkhaniyi kwa abale ake ndipo bambo ake atayang’ana pamene amasungapo mfuti yawo sanayipeze, zomwe zinachititsa kuti ayambe kumufufuza mpaka atampeza pamalo ena atafa, pambali pake pali mfuti ndi lamya yake.

Achipatala atapima thupi la malemuwa apeza kuti Tinasha anafa chifukwa cha mabala a m’mutu chifukwa cha chipolopolo.

Mtawali adali wa m’mudzi wa Senzani m’boma la Ntcheu.

 

Related posts

Four suspects in cooler over motorcycles theft

Romeo Umali

Over 29,000 students’ loan applications filed at Loans Board

Romeo Umali

Entrepreneurship skills key in youth development — TEVETA

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.