Malawi Broadcasting Corporation
Crime Nkhani

Mayi wathawa atatentha manja a mwana wake

Apolisi ku Mangochi akufunafuna mayi Gladys Lingoni amene wathawa pomuganizira kuti watentha manja a mwana wake wa zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa anadya ndiwo za soya zomwe anakonza kuti adyere msima.

Ofalitsankhani za polisi ya Mangochi, Amina Tepani, Daudi wati Lingoni ndi wammudzi mwa Sadibwa mdera la mfumu yaikulu Mkanda m’boma la Mulanje.

Panopa apolisiwo akupempha anthu akufuna kwabwino omwe angadziwe komwe mayiyo wabisala kuti awadziwitse chifukwa wasiyanso ana ena pakhomo pake.

Olemba Davie Umar.

Related posts

Mayi Monica Chakwera atsogolera amayi pa mapemphero a tsiku la a mayi

Rabson Kondowe

THREE NABBED FOR CRIME IN MZIMBA

Rabson Kondowe

Makolo asiya mwana pa golosale

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.