Mkulu woona za zamaphunziro a zachuma ku Old Mutual a Bernard Chiluzi ati anthu ambiri amene akukhuzidwa ndi mchitidwe odzipha m’dziko muno akuchita izi kaamba ka mavuto a zachuma.
A Chiluzi anena izi ku Lilongwe pa mwambo okhazikitsa bungwe la Rhema Manifest lomwe ati lidziika pamodzi achinyamata a mipingo yosiyanasiyana ndikuwaphunzitsa zokhudza moyo kuphatikizapo zachuma.
Mneneri Patson Gondwe yemwe wayambitsa guluri wati ndizomvetsa chisoni kuti achinyamata mumipingo saphunzitsidwa mbali zonse za moyo, zomwe zikuchitsa kuti anthu adziyang’anira pansi mipingo poganiza kuti anthu opemphera amayenera kukhala osauka.
“Sizoona kuti anthu akaona munthu opemphera ali ochita bwino adziganiza kuti ndi opembedza satana. Tikufuna achinyamata akhale odzidalira paokha powaphunzitsa mbali zonse za moyo,” anatero a Gondwe.
Pamwambowu panali akuluakulu a mabungwe, a zamalamulo, a katswiri oyimba nyimbo zauzimu komanso akuluakulu a mipingo yosiyanasiyana.