Bungwe la alimi a fodya la TAMA Farmers Trust layamikira mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera poonetsetsa kuti alimi a fodya akugulidwa fodya pa mitengo ya bwino chaka chino.
Mtsogoleri wa bungweli, a Kalima Banda, ayankhula izi ku nyumba ya chifumu mu mzinda wa Lilongwe pamene alimi a fodya a m’bungweli anakumana ndi Dr Chakwera.
A Banda anapempha kuti boma liwathandize pokwanilitsa chiwerengero cha makilogaramu a fodya yemwe ogula akumufuna. Iwo anati ndi zosangalatsa kuona kuti alimi akukondwa ku msikawu kaamba ka mitengo yabwinoyi.
Mwazina, iwo anati anakakonda kuti mtsogoleri wa dziko linoyu apitilize kuthandiza poonetsetsa kuti alimiwa adzilandira ndalama zafodya yemwe agulitsa mmisika ya fodya pakangotha masiku awiri okha.