Lero masana ikamakwana 2:30, matimu a Silver Strikers ndi Mighty Mukuru Wanderers athambitsana pabwalo la Silver mu mzinda wa Lilongwe.
Silver, yomwenso imatchedwa kuti Mabanker, ili pamwamba pa mndandanda wa matimu amu ligi yayikulu ndi ma point 16 pomwe Wanderers, yomwe imadziwikanso kuti Manoma, ndi yachinayi ndi mapoint 12.
Matimu onsewa sadagonjeko mu ligiyi ndipo m’modzi mwa ochemelera, Gogo Duzu Munthali, amene achokera m’boma la Karonga, ati masewerowa ndi obvuta zedi.
“Awa simaseworo ophweka, chichitike pano tivomereze basi,” a Duzu, amene amachemelera Mabanker komanso ali ndi zaka 91, anafotokoza.
Matimuwa akumana kokwana ka 26 mu ligiyi ndipo Manoma ndi amene apambana kwambiri popeza anakwanitsa kutidzimula Mabanker ka khumi ndi kamodzi, pomwe anzawowa akwanitsa kasanu ndi kanayi komanso kufanana mphamvu kasanu ndi kamodzi.