Malawi Broadcasting Corporation
Education Local Local News Nkhani

LUANAR itha kukwanilitsa masomphenya a Malawi 2063

Nduna yoona za maphunziro asukulu za ukachenjede, a Jessie Kabwila, yati sukulu ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (LUANAR) ndi yofunika kwambiri pokwanilitsa masomphenya a Malawi 2063.

A Kabwila amayankhula izi pamene anayendera zitukuko zosiyanasiyana zimene sukuluyi ikuchita.

Iwo anatamanda mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, chifukwa chokhazikitsa ntchito ya minda ikuluikulu imene ikuthandizira nkhani yakuti alimi azitenga ulimi ngati malonda.

Ndunayi inati LUANAR ikugwila ntchito yayikulu yoonetsetsa kuti ulimi wa somba upite patsogolo.

A Kabwila anati pa ulendowu anali ndi mwai ofotokoza za bilo yokhudza sukulu zaukachenjede imene akuyembekezera kuti aphungu a nyumba ya malamulo akayisayine.

Vice Chancellor wa LUANAR, Professor Emmanuel Kaunda, anati apitiriza kugwira ntchito zosiyanasiyana zakafukuku pofuna kukwanilitsa masomphenya a Malawi 2063.

 

Related posts

Civil thumps Hammers

Romeo Umali

Ophunzira apindilana ndebvu mkamwa

Rabson Kondowe

T/A Amidu alowa mmanda

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.