Malawi Broadcasting Corporation
Local News Nkhani Sports

Kodi ndi Arsenal kapena Manchester City?

Lero ndi tsiku lokwangula ligi ya ku Engalnd pamene m’modzi mwa matimu a Arsenal ndi Manchester City avekedwe ufumu wa ligiyi.

Manchester City ndi imene ili pamwamba ndi ma point 88 ndipo Arsenal ndi yachiwiri ndi ma point 86.

Masewero omaliza ali motere:

Manchester City ionetsana chamuna ndi West Ham pa bwalo la Eitihad, pomwe Arsenal ithambitsana ndi Everton pa bwalo la Emirates.

M’ndandanda ukuoneka chonchi

Ndi m’mene zililimu, kuti City itengenso ukatswiri kwa kanayi motsogozana, ingopambana basi, koma kuti Arsenal inyamule chikhochi, iyenera kuti ikwapule Everton komanso ipemphere kuti West Ham igonjetse kapena ifanane mphamvu ndi anyamata ovala za mtambo aku Manchester.

Masewero onsewa akhala akuchitika kuyambira 5 koloko madzulo.

 

Related posts

Self-help initiatives springing up in Mwanza

Alinafe Mlamba

Mphunzitsi amumanga ataba ndalama za mayeso

Rabson Kondowe

Govt calls for collective efforts to end child marriages

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.