Anyamata awiri, Dziwani Mwachumu ndi Kenneth Banda, adzitama kuti apalasa njinga kuchokera mumzinda wa Lilongwe kukathera mumzinda wa Blantyre kwa masiku awiri.
Iwo ati achita zimenezi kuyambira Lolemba mpakana lachiwiri ndipo akufuna kutolera ndalama yokwana K100 million imene idzagwire ntchito yothandizira anthu amene anakhudzidwa ndi El Nino komanso ngozi zina zogwa mwadzidzi.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Saulos Chilima, adzawaperekeza anyamatawa, bungwe la Malawi Red Cross Society latsimikiza.
Ofalitsankhani ku bungweli, a Felix Washoni, ati mwambowu ukakhala mbali imodzi yofuna kudziwitsa anthu ntchito imene amagwira modzipeleka.
Iwo anati izi ndikutsatira mapazi a mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, amene adakhazikitsa sabata yokumbukira anthu ogwira ntchito mongodzipereka pothandiza anthu.
A Washoni ati paulendo opalasawu iwo adzathandiza bungwe la Malawi Blood Transfusion kutolera magazi.