Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Kamtukule alowa chipani cha MCP

Nduna ya zokopa alendo a Vera Kamtukule omwe anali achipani cha UTM alowa chipani cha Malawi Congress.

Powalandira mchipanichi Mlembi Wamkulu mchipani cha MCP a Eisenhower Mkaka ati a Kamtukule sanasochere kaamba koti alowa chipani chomwe chilibe mwini koma mchipani cha m’Malawi aliyense.

A Mkaka ati chipani cha MCP chili chokonzeka kulandira aliyense yemwe watsimikiza mtima kulowa chipanichi.

Poyankhulapo a Kamtukule ati alowa chipanichi kaamba koti akufuna kuthandiza mtsogoleri wadziko lino  Dr Lazarus Chakwera pogwira ntchito yotukula dziko la Malawi.

 

Related posts

Demand quality works –– Chomanika

MBC Online

MCP ikufuna zipani zidzichita misonkhano mwaufulu

Rabson Kondowe

District councils urged to enforce spatial plans for development

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.