Nduna yaza mtengatenga, a Jacob Hara, yati sitima yoyenda pakati pa mizinda ya Blantyre ndi Lilongwe iyambiranso posachedwapa.
A Hara anati gawo lachiwiri ikhala kukonzanso njanji yolowera m’boma la Mchinji pofuna kulumikizitsana ndi dziko la Zambia.
Iwo ati izi zili chomwechi chifukwa akonza mlatho omwe unaduka zomwe zichititse kuti sitima iyambenso kuyenda.
Olemba : Patrick Dambula