Wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), a Justice Annabel Mtalimanja, wapempha aMalawi kuti achotse chikayiko chimene angakhale nacho pa makina amakono akalembera wamavoti.
A Mtalimanja anena izi pamene gawo lachitatu lakalembera wa m’kaundula wachisankho wayamba m’madera ena a m’maboma a Lilongwe, Mchinji, Mangochi, Chikhwawa, Nsanje ndi Mzimba.
Iwo anatu, “anthu ena akuganiza kuti makinawa ndi ovotera kapena kubera zisankho, ayi. Taonani sipanathe mphindi ziwiri ine ndalembetsa.”
Wapampandoyu anapemphanso zipani za ndale kuti zikhale patsogolo kuwunikira anthu zokhudza ubwino olembetsa m’kaundulayu.