Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Dr Chakwera ayamikira anthu ku Nsanje posamukira kumtunda

Prezidenti Dr Lazarus Chakwera wayamikira anthu aku Makhanga m’boma la Nsanje kaamba kosamukira kumtunda pothawa madzi omwe akhala akuwasautsa chaka chilichonse.

Mtsogoleriyu wayamikiranso aphunzitsi polimbikira ntchito ndikumakhonzetsa ana kupita ku university, ngakhale anali atathawa msukulu zawo chifukwa cha namondwe.

Dr Chakwera amayankhula ku Makhanga komwe ayendera ntchito yomanga sukulu zatsopano.

Prezidenti Chakwera wati akumananso ndi bungwe la Give Direct, lomwe lathandiza midzi ina ku Makhanga kumanga nyumba anthu atathawa kunyumba zawo kaamba kamadzi.

Dr Chakwera wati akumananso ndi akuluakulu a bungweli kuti atsirize midzi itatu komanso kumanga sukulu yomwe inatsala.

Chaka chatha, Dr Chakwera anakumana ndi mkulu wa bungweli pomwe anapita ku America, zomwe zinathandiza kuti abwere kudzamanga nyumbazi.

Dr Chakwera ayenderanso chipatala cha Osiyana m’boma lomweli la Nsanje.

 

Olemba: Mercy Zamawa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Govt. boosts food security at Nkhata Bay Prison

MBC Online

Beach Soccer Malawi saddened by Kaluwa’s demise

Rudovicko Nyirenda

Government empowers 111 youths in Neno

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.