Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Chitetezo munthawi ya chisankho ndi chofunika

Msonkhano wa akuluakulu a m’maboma mchigawo chakumpoto uli mkati komwe nkhani yaikulu ndi ya chitetezo panthawi ya chisankho, chomwe chichitike chaka chamawa.

Poyankhula pamene amatsekulira msonkhanowu, mmodzi wa makomishonala abungwe loyendetsa chisankho m’dziko muno la MEC, a Anthony Mukumbwa, ati chisankho sichingayende bwino ngati palibe chitetezo chokwanira.

Iwo ati ichi ndi chifukwa chake malamulo atsopano achisankho ayika udindo waukulu wa chitetezo kwa akuluakulu apolisi am’maboma.

“Tikukumana ndi ma DC am’maboma komanso akuluakulu apolisi ndicholinga chakuti adziwe udindo omwe ali nawo pankhani zachitetezo ndi zina, malinga ndi malamulo atsopano oyendetsera chisankho,” a Mukumbwa anafotokoza.

Kumsonkhanowu kuli ma DC amaboma onse achigawo chakumpoto komanso akuluakulu a polisi mchigawochi.

 

Wolemba: Henry Haukeya

Related posts

Titolera ndalama zokwana K2.18 trillion chaka cha 2023/24 — MRA

Romeo Umali

‘Akabaza kalembetseni m’kaundula wa voti’

Romeo Umali

SATCP advances infrastructure plans

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.