Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Nditha kusiyira sukulu panjira — Mphatso

Mnyamata wina, Mphatso Sidiki, wadandaula kuti atha osalemba nawo mayeso aboma a Form 4 ngati sipapezeka ena omuthandiza kulipira nyumba yokhalamo komanso school fees, zonse zokwana K200,000.

Nkhani ya Sidiki ndiyomvetsa chisoni kuchokera kumudzi kwawo kumene adamusankhira pa secondary yoyendera ya Chinamvuuwu kwa Lundu ku Blantyre pomwe ena anamuuza kuti athawe kumudziko poopa kuti ena angamuchite chipongwe kamba ka khungu lake.

Iye wati anthuwa anamulonjeza kuti alembera ku unduna wazamaphunziro kuti amupititse ku sukulu yogonela komko, zomwe sizinatheke koma atafika kale ku Bangwe mumzinda wa Blantyre.

Mnyamatayu, yemwe ndi wa zaka 17, wati amakhala yekha nyumba ya renti ku Bangwe komwe anangoyamba sukulu yomwe siyaboma, ndipo nyumbayo amalipira K15 000 pamene sukuluyi akuyenera kulipiranso K50 000, ndipo pamodzi akuyenera kukhala ndi K200000 kwacha kuti adzafike tsiku lotsiriza kulemba mayeso a MANEB m’mwezi wa July chaka chino.

Mphatso wapempha akufuna kwabwino kuti amuthandize kuti alembe mayeso kamba koti akulingalira zongobwelera kumudzi kwa Lundu kuti akakhale pansi, zomwe zisokoneze malingaliro ake odzakhala namwino.

Ofuna kumuthandiza, iye wati angamupeze pa 0899623449.

#MBCDigital
#Manthu

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

First Lady visits Mzuzu Government Secondary School

Romeo Umali

Ekhaya, Blue Eagles akwapulana la mulungu

Yamikani Simutowe

All set for Top Product Awards 2024

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.