Bungwe la Malawi Council of Disability Affairs (MACODA) lapempha olembankhani m’dziko muno kuti adzilemba nkhani zomwe zingalimbikitse ufulu wa anthu omwe ali ndi ulumali.
Mkulu wabungweli, a George Chiusiwa, anena izi m’boma la Salima pamaphunziro a olembankhani, omwe cholinga chake ndi kuwapatsa upangiri oyenera okhudza anthu aulumali kuti adzitha kufotokozera bwino aMalawi zambiri zokhudza ufulu wa anthu a ulumali.
Malinga ndi a Chiusiwa, bungwe la MACODA, lomwe kale limadziwika kuti MACOHA, panopa liri ndi mphamvu yolandira madandaulo komanso kufufuza milandu yokhudza anthu aulumali omwe ufulu wawo waphwanyidwa, potengera lamulo latsopano lokhudza za ulumali.
A Chiusiwa alimbikitsanso anthu m’dziko muno kuti adzitsata ndondomeko za mu lamuloli, zothandiza kuchepetsa mavuto omwe anthu a ulumali amakumana nawo akafuna kugwira ntchito zosiyanasiyana monga kumanga nyumba komanso kuika zipangizo zoyenera kuti anthu aulumali adzitha kufikamo mosavuta.
Maphunzirowa akuchitika ndi thandizo lochokela ku bungwe la World Vision Malawi kudzera ku project yomwe ikudziwika kuti Able to Thrive.