Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Chisankho chayenda bwino’

Wapampando wa bungwe loona za chisankho la Malawi Electoral Commission, Justice Annabel Mtalimanja, wati ndi okhutira ndi mmene chisankho chapadera chayendera m’maboma a Mangochi ndi Blantyre.

Iwo ati panalibe mavuto odetsa nkhawa kupatula kuti anthu ena amabwera ndi chaunzika kuti adzavote.

“Pamene tikukonzekera chisankho cha chaka cha mawa, aMalawi akuyenera kudziwa kuti chiphaso cha unzika sichoponyera voti, koma akuyenera kulembetsa kuti adzathe kuponya voti,” iwo anatero.

Chisankho chapaderachi chachitika ku ma Ward a Chilaweni m’boma la Blantyre ndi Mwasa m’boma la Mangochi.

Pakadali pano, ntchito yowerenga mavoti yayamba.

Bungwe la MEC  lilengeza zotsatira za chisankhochi mawa pa 24 July 2024 ku Holo ya HHI munzinda wa Blantyre.

 

Olemba: Secret Segula ndi Arthur Chokhotho

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

GOVT LAUDS MARANATHA ACADEMY

McDonald Chiwayula

Govt, NGOs urged to collaborate for Malawi 2063

MBC Online

Quech Nursing Officer urges support for patients

Chisomo Break
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.