Chipatala chatsopano cha Namatuni chatha tsopano, Mfumu Nguluwe yadera limene kuli chipatalachi kwa Inkosi Bvumbwe m’boma la Thyolo, ndi imene yatsimikiza.
Mfumu Nguluwe yati chipatalachi chithandiza pochepetsa imfa zimene zimadza kaamba ka kutalikirana ndi chipatala.
Mfumuyi yati anthu atatu anamwalira akupita nawo ku chipatala chaku boma chaka chatha mderali mutabuka matenda a cholera.
Kudzera ku thandizo la ndalama lochokera ku World Bank pansi pa GESD, boma lamanga chipatalachi pamodzi ndi nyumba ya ogwira ntchito zachipatala pamalopa.