Apolisi agwira nzika yaku Niger pabwalo la ndege la KIA itabisa mankhwala woopsya kumalo wochitira chimbudzi.
Apolisi apabwaloli ati Osman Mohamed, amene ndiwa zaka makumi atatu, anapezeka ndi mankhwala wozunguza bongo a diamorphine – heroin olemera pafupifupi 1 kilogramme.
Malinga ndi ofalitsankhani wa apolisi ku KIA, a Dorrah Machila, Lachiwili Mohamed amayembekezeka kukwela ndege ya Ethiopian Airlines pa ulendo wopita m’dziko la Germany pomwe apolisi anamuchita chipikisheni.
Malinga ndi a Machila, apolisi anamupatsa madzi akumwa wotentha, zomwe zinachititsa kuti atulutse mibulu 51 ya diamorphine yomwe anaiika kumalo okhalirawo.
Malinga ndi a Machila, panopa apolisi amutsekulira Muhamed mlandu wopezeka ndi mankhwala woopsya wozunguza bongo ndipo akuyembekezeka kukaonekela kubwalo la milandu posachedwapa.