Timu yampira wamanja ya Blue Eagles tsopano yapereka chikho cha One NICO top 12 kwa mkulu wa apolisi mdziko muno itapambana chikhochi lamulungu lapitali mumzinda wa Lilongwe.
Unali mwambo ochititsa chidwi pomwe atsikana alusowa amaguba mwamanyado, ulendo okasiya chikhochi m’manja mwa mkulu owona za kafukufuku komanso mapulani, a Dennis Chipawo, omwe alandira chikhochi mmalo mwa mkulu wa apolisi, a Richard Luhanga.
Ndipo a Chipao ati kufika kwachikhochi kwaonjezera chisangalalo cha kulandiridwa kwa mkulu wa apolisi watsopanoyu, yemwenso amakonda kwambiri masewero.
Iwo alonjeza kuti nthambi ya apolisi ipitilira kupereka thandizo ku timuyi kuti ipitilire kuchita bwino m’mipikisano yosiyanasiyana.
Mtsogoleri wa osewera a timu ya Blue Eagles, Molly Chisambiro,
watsimikizira akuluakulu atimuyi kuti apitilira kudzipereka ndikusunga mbiri yabwinoyi.
Mlembi wamkulu wa bungwe la Netball Association of Malawi, Yamikani Kauma, wayamikira nthambi ya polisi kaamba ka chidwi chake chothandiza kutukula masewero osiyanasiyana, kuphatikizapo mpira wamanja.
Timu ya Blue Eagles ndiyo ikuteteza zikho za Salima Sugar komanso One NICO pomwe timu yake yaing’ono ya Young Eagles ikuteteza chikho cha mchigawo chapakati cha MPICO.
Olemba: Foster Maulidi


