Nthambi yoona za usodzi yachita mgwirizano ndi mabungwe a asodzi ang’onong’ono m’maboma a Nkhatabay ndi Nkhotakota pofuna kuwapatsa mphamvu ndi umwini poteteza nsomba mu nyanja ya Malawi.
Mkulu oona za usodzi m’dziko muno, Hastings Zidana, ati mgwirizanowu uthandiza kuti nsomba zichuluke mu nyanjayi komanso pakufunika ndondomeko zoyoyenera mu gawo la usodzi.
Malinga ndi a Zidana, nyanja ya Malawi ikutulutsa nsomba zokwana matani 180,000, zomwe ndi zoyandikana ndi masomphenya a boma pofuna kukwanitsa kuti chiwerengerochi chikwane 350,000 metric tonnes pofika chaka cha 2030.
Mkulu wa bungwe la Ripple Africa, a Force Ngwira, ati iwo apitiriza kugwira ntchito zosiyanasiyana zokhudza usodzi mpaka anthu atasintha kaganizidwe ndikuyamba kusamala nsombazi.