Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Band yanyimbo zauzimu yadziko lonse ibwera poyera

Gulu la akatswiri oyimba nyimbo zauzimu  osachepera 50 amene adakumana koyamba mu 2020, tsopano akhazikitsa Hephzibah Worship Band.

Malinga ndi mkulu wa gululi a Peterson Nachanje, cholinga cha gululi ndi kusula komanso kutukula luso lamayimbidwe auzimu.

“Sitikusiyana kwenikweni ndi Joyous Celebration yaku South Africa. Sitikuona mpingo koma luso lamunthu, kaya amatha kuimba zida kaya mawu, ali olandiridwa abwere,” atero a Nachanje.

M’modzi mwa otsogolera gululi ndi Good Friday, yemwe anatchuka ndi nyimbo yoti ‘Wanga ndili Naye’ ndipo wati gululi linayamba kujambula chimbale m’chaka cha 2021 ndipo pofika lero lajambula akanema atatu apamwamba.

 

Wolemba: Emmanuel Chikonso

Related posts

APM Seeks Tony Blair’s Support in Mining, Energy Investments

Austin Kakande

Over 262, 000 students sit for 2024 PSLCE exams

Romeo Umali

Seven percent in Malawi living with diabetes

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.