Oyimba wamkazi Puleng Phoofolo pamodzi ndi munthu wina amene amayendetsa galimoto ali m’chipatala cha Boitumelo m’dziko la South Africa kutsatira ngozi imene achita dzulo masana ku Free State m’dzikolo.
Oyimba odziwika bwino Malome Vector, Lizwi Wokuqala pamodzi ndi katswiri ojambula makanema Da Mos ndiwo afa pangoziyi.
Koma malipoti a ku South Africa akutsutsa kuti oyimba Wave Ryder ndi Ntate Stunna anali anali nawo pangoziyo.
Anthu asanuwa anali pa ulendo okajambula kanema wa nyimbo yawo yatsopano pomwe galimoto limene anakwera linaphulika tayala ndipo linakaombana ndi galimoto lamtundu wa truck.