A Polisi m’boma la Chiradzulu anjata a John Mapoko a zaka 30 omwe ndi m’phunzitsi pa sukulu ya pulaimale ya Mulirankhwali kaamba kowaganizira kuti anachita zadama ndi mtsikana wa zaka 16 za kubadwa.
Malingana ndi m’neneri wa polisiyi, a Cosmas Kagulo, a Mapoko anapalana ubwenzi wa mseli ndi mtsikanayu ndipo abale ake ndi amene anakawaneneza ku polisi atawaona akutulukira m’munda wina kumeneko.