Malawi Broadcasting Corporation
Local News

A Chakwera akutsogolera aMalawi pa mapemphero okumbukira ufulu wa dziko lino

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, lero akutsogolera mtundu wa aMalawi pa mapemphero apadera okondwelera kuti dziko la Malawi lakwanitsa zaka 60 pa ufulu odzilamulira.

Pamwambowu palinso wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, atsogoleri a mipingo yosiyana, nduna za boma ndi akazembe amaiko ndi mabungwe osiyanasiyana.

A Chakwera ndi amene adalamula kuti chaka chino pasakhale zochitikachitika monga zimakhalira nthawi zonse koma mapemphero okha chifukwa cha ziphinjo zomwe dziko lino lakumana nazo, kuphatikizapo imfa ya amene anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu.

Pa mwambowu, omwe ukuchitikira ku BICC mu mnzinda wa Lilongwe, anthu anakhala chete mphindi imodzi pokumbukira ndikupereka ulemu kwa malemu Dr Saulos Chilima ndi ena asanu ndi atatu.

Mutu wa Mapempherowa ndi ‘Kuyenda limodzi mochilimika’.

 

Olemba Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

INTERNATIONAL RED CROSS SG MEETS PRESIDENT CHAKWERA

MBC Online

EU unlocks K174 billion for Malawi

MBC Online

Wanderers leads the pack!

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.