Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Aphwanya malamulo la chipani cha UTM— Kondowe

Mkulu oona za chisankho ku chipani cha UTM, Happy Kondowe, wati zomwe achita mamembala ena achipanichi kulengeza tsiku la pa 17 November chaka chino ngati lomwe adzachite msonkhano waukulu wa chipanichi ndikuphwanya malamulo.

Malinga ndi a Kondowe, ngakhale mtsogoleri wa UTM, Dr Michael Usi, anali nawo pazokambirana zofuna kukhazikitsa tsiku la msonkhanowo, mamembalawo amayenera kumvana ndi komiti yaikulu asanalengeze za tsikuli.

A Kondowe anena izi potsatira msonkhano wa atolankhani umene mneneri wachipanichi, a Felix Njawala pamodzi ndi mlembi wamkulu wachipanichi, a Patricia Kaliati anachititsa mu mnzinda wa Blantyre wolengeza za tsikuli.

Ku msonkhanowo, a Kaliati komanso a Njawala anati alengeza za tsikuli potsatira zokambirana zimene adachita ndi mamembala achipanichi, kuphatikizapo Prezidenti wawo Dr Usi yemwe anati anavomereza za tsikuli.

Koma a Kondowe ati ngakhale kuti Dr Usi analipo, mamembalawa afulumira kulengeza komiti yaikulu isanavomereze.

Malinga ndi a Kondowe, chipani cha UTM sichikugwirizana ndi zomwe alengeza mamembalawo.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Women journalists urged to use AI professionally

Lonjezo Msodoka

Ntchito za manja zikuthandiza kusintha miyoyo ya achinyamata

Doreen Sonani

‘Boma ligwirane manja ndi opanga fetereza wa Mbeya’

Paul Mlowoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.