Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Amulamula akagwire ndende yakalavula gaga chifukwa chopezeka ndi chida choopsa

Bwalo lamilandu ku Mangochi lalamula Boika Sabiti wazaka 48 kuti akakhale ku ndende zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa chopezeka ndi chida choopsa chopangidwa ndi zitsulo zosongoka komanso zakuthwa.

Boika adamumanga usiku wapa 19 August, 2024.

Mkati kati mwamulanduwo, Boika adakanika kufotokoza bwino lomwe chifukwa chenicheni chimene amasungira chida choopsacho mchikwama mwake. Ngakhale ananena kuti chinali chophera Ng’ona, bwalolo linaunikira umboni wakuti iyeyo alibe udindo okupha Ng’ona, zimene ndi zotetezedwa ndi malamulo.

Kumbali yawo, apolisi anati Boika, amene ndi kabwere-bwere ku ndende, sakuonetsa kusintha kulikonse ndipo anapempha chilango chokhwima.

Oweruza milandu Baxter Chikalimba anapereka chilangocho kuti ena atengerepo phunziro

Related posts

Komiti yakunyumba yamalamulo yakhutira ndikuthetsedwa kwa mlandu wa a Chilima

Rabson Kondowe

Tikambe zabwino za dziko lathu — JB

Romeo Umali

‘Mtayakhasu ndi ulimi othana ndi njala’

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.