Bungwe la alimi m’dziko muno la Farmers Union of Malawi (FUM) lapempha mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, kuti awathandize kupeza misika mosavuta.
Mtsogoleri wa bungweli, a Maness Nkhata, amalankhula izi ku nyumba yaboma munzinda wa Lilongwe kumene iwo amakumana ndi Dr Chakwera.
Mwa zina, a Nkhata anati anakakonda kuti bungwe la National Food Reserve Agency (NFRA) likhale ndi makina owumitsira chimanga chifukwa chimanga chambiri chikumabwezedwa.
Iwo anayamikiranso mtsogoleri wa dziko lino poikirapo mtima pokweza ntchito za ulimi m’dziko muno, kuphatikizapo kuyambitsa ulimi wa minda yaikulu ya Mega Farms.
A Nkhata anapemphanso kuti pakhale mwayi oti alimi adzipeza mpata wopatsidwa ngongole kuchokela ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF).
Alimi osiyanasiyana ochokera m’maboma onse m’dziko muno ndi amene anakumana ndi Dr Chakwera ku Lilongwe, pansi pa bungwe la FUM.