Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Adindo azipembedzo apemphelera dziko la Malawi

Adindo azipembedzo zosiyanasiyana m’dziko muno lero asonkhana ku Mponela m’boma la Dowa kumene akupempherera dziko la Malawi komanso atsogoleri ake. 

Iwo, n’kupemphera kwawo, akuthokoza zimene Mulungu wakhala akuchitira dziko lino ndi kupempherera kuti Mulungu apitirize kudalitsa dziko lino ndipo apemphereranso kuti mvula ya chaka chino igwe bwino m’madera onse.

Iwo mmapemphero awo akutsutsananso ndi maganizo komanso mizimu yoipa monga ngozi zimene zakhala zikuchitika m’dziko muno.

Pokonzekera zisankho zimene zikudza chaka cha mawa, adindowa akupemphereranso kuti dziko lino lidzakhale ndi zisankho zabata ndi mtendere.

Mapemphero amtunduwa akuti akuchitika m’maboma osiyanasiyana ndipo apitilira kuchitika.

Related posts

Zomba DC urges popularisation of contingency plan

Romeo Umali

BWANJI SIMUNANENE?

MBC Online

DPP’s 2014-2020 era was economically stable — Mwanamvekha

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.