Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports Sports

Mpikisano wa 1 NICO Netball watentha

Ntchito yodzipezera malo mu ndime yadziko lonse mumpikisano wa 1 NICO Netball m’chigawo chapakati tsopano yafika pachimake pamene matimu a CIVO Nets ndi Blue Eagles Sisters afika mu ndime yotsiriza.

Timu ya Blue Eagles ndiyo inali yoyamba kufika mu ndime yotsirizayi itagonjetsa Young Eagles yomwe ndi timu yake yaing’ono ndi zigoli 50 ku 41 pomwe CIVO yagonjetsa MDF Lionesses ndi zigoli 55 kwa 50.

Padakali pano, Young Eagles ndi MDF akusewera mu ndime yofuna malo achitatu, isanayambe ndime yotsirizayo pomwe katswiri atenge chikho ndi ndalama zokwana K1 million.

Matimu atatu ndi omwe adzigulire malo mu ndime yadziko lonseyi m’chigawo chapakati ndipo adzakasewera ndi matimu ena akummwera komanso kumpoto.

Related posts

Govt records K21 billion surplus in January

Rabson Kondowe

Artists still paying Martse homage

Romeo Umali

NEW LILONGWE BRIDGE SOON – ROADS AUTHORITY

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.