Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

A Mwakasungula ati bajeti ili bwino zedi

Mmodzi mwa anthu amene amayankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana, maka zolimbikitsa ulamuliro wabwino, a Undule Mwakasungula, ati dongosolo la zachuma lomwe alipereka mnyumba ya malamulo lachisanu a nduna a zachuma, a Simplex Chithyola Banda, ndi mbambande.

Iwo ati ndondomekoyi ithandiza kutukula miyoyo ya anthu m’dziko muno.

A Mwakasungula anena izi a Banda atapereka ndondomeko yazachuma yachaka chino kufikira chaka chamawa ya ndalama zokwana K5.9 trillion.

A Mwakasungula ati dongosolo latsopanoli laonetseratu kuti boma laika chidwi pantchito yotukula miyoyo ya a Malawi.

Related posts

Nduna yazofalitsa nkhani ipereka lipoti la ngozi ya ndege ya Chichewa

Romeo Umali

Madzi aukhondo afika ku Mphampha ndi Tsambalabooka m’boma la Chikwawa

Romeo Umali

Osewera watsopano wa Wanderers Tanjong apezeka kumathero asabatayi

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.