Apolisi ku Chiradzulu amanga mphunzitsi wazaka 36, Daniel William, wa pa sukulu ya pulayimale ya Chawe pomuganizira kuti anaba ndalama zokwana K67,150 zolipilira mayeso a sitandade 8.
Ndalamazo akuti zinali za ophunzira 17.
Ofalitsankhani wapolisi ku Chiradzulu, Cosmas Kagulo, wati mphunzitsiyo anamusankha kuti atolere ndalama za mayeso kuchokera kwa ophunzira a sitandade 8 pasukulupo ndipo awalipilire kudzera pa foni.
Koma ophunzira ena anadabwa kuti tsiku lopereka ziphatso za ma ID zolembera mayeso, maina awo panalibe.
Akuluakulu pasukulupo atamufunsa, mphunzitsiyo anavomera kuti anagwiritsa ntchito ndalamazo njira zina.