Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

A Chilima adatukula kampani yathu ya Airtel — Kamoto

Mkulu wa kampani ya Airtel Malawi, Charles Kamoto, wati malemu Dr Saulos Chilima anali munthu wodzipereka ndi wokonda ntchito.

Poyankhula ndi MBC, a Kamoto ati kampani ya Airtel Malawi sidzaiwala zazikulu zomwe adachita posintha kagwilidwe ka ntchito kumpaniyi.

“Ma tower ambiri omwe mukuwaona m’dziko muno a Airtel, malemu a Chilima ndi omwe adathandizira kuti ayike malo osiyanasiyana,” anatero a  Kamoto.

Iwo anati adaphunzira zinthu zambiri kuchokera kwa malemu Dr Chilima.

Malemu Dr Chilima adagwilako ntchito ku kampani zosiyanasiyana m’dziko muno, kuphatizapo Airtel Malawi, asadayambe kuchita za ndale.

 

Related posts

Bullets extend Babatunde loan deal

Romeo Umali

‘Andale ena akumatenga anthu ammadera akutali kudzawalembetsa mkaundula wa voti’

Rabson Kondowe

Malawi charts path to Climate-responsive Migration Policy

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.