Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Andale ena akumatenga anthu ammadera akutali kudzawalembetsa mkaundula wa voti’

Mmodzi mwa omwe akufuna kupikisana nawo pa udindo wa phungu mdera la Mangochi Municipal pachisankho cha chaka cha mawa, Anussah Daddy Hassein, wadandaula ndi mchitidwe wa andale ena, amene akuti akutenga anthu ammadera akutali ndikukawalembetsa mdera la town ya Mangochi.

A Hassein, omwe akuimira chipani cha Malawi Congress (MCP), apereka dandauloli  lero pamene amakalembetsa mkaundula wa voti ku centre ya Mangochi Municipal.

“Ndondomeko ya kalembera wa voti ikuyenda bwino palibe chovuta, koma chomwe tikudandaula ndichakuti anthu ena a ndale akumatenga anthu akutali kubwera kudzawalembetsa mkaundula wa voti kuno constituency ya town ya Mangochi sitikudziwa cholinga chawo kuti ndi chani,” anatero a Hassein.

Koma yemwe akuyang’anira ntchito yakalembera wa voti pa municipality ya Mangochi, Martin Kuyere, ati pakadali pano dandauloli silinawapeze.

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) liri mu gawo lachitatu la kalembera wa voti lomwe layamba pa 28 November 2024.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mphenzi yapha asodzi awiri ku Mangochi

Davie Umar

Senior Chief Kapoloma dies

MBC Online

Puma partners Blue Elephants in symbiotic deal

Earlene Chimoyo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.