Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

‘A Chakwera ataya kholo mu uzimu’

Mlangizi wa prezidenti pa ndale a Kingsley Sulamoyo ati mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wataya kholo mu uzimu pa imfa ya the Very Reverend Killion Mgawi.

A Sulamoyo, omwe ayankhula mmalo mwa Dr Chakwera, ati panthawi yomwe mtsogoleri wa dziko linoyu anali pa sukulu ya ubusa, anakhala limodzi ndi abusa a Mgawi ndipo amawalangiza ndi kuwaunikira m’magawo osiyanasiyanasiyana.

A Sulamoyo ati Dr Chakwera ndiothokoza kuti abusa a Mgawi asiya anthu odalirika omwe akugwira ntchito zikuluzukulu mothandizana ndi a Prezidenti kuyendetsa dziko lino.

Iwo apempha a Malawi kuti aphunzire pa momwe abusa a Mgawi akhalira moyo wawo pa dziko pano.

Mtsogoleri wa dziko lino wapepesa banja la a Mgawi pa imfayi ndi ndalama yokwana K2 million.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Matenda a Kadzamkodzo ndi ochizika’

Lonjezo Msodoka

Mayi amangidwa poganiziridwa kuti wapha mwamuna wake

Romeo Umali

MCP yayamikira anthu aku Mangochi powakhulupilira

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.