Chataika Makawa wazaka 45 ali mchitokosi cha polisi ku Mangochi pomuganizira kuti wapha mkazi wake Esimy Daudi wazaka 42, amene amamukayikira kuti anali ndi chibwenzi.
Ofalitsankhani za polisi ya Mangochi, Amina Tepani Daudi, wati Makawa amumanga mmudzi mwa Kwitunji mdera la mfumu yaikulu Katuli dzulo pomuganizira kuti wapha mkazi wakeyo pomubaya ndi chikwanje kumsana.
Daudi wati mukafukufuku wawo, apolisi apeza kuti banjali linali lapendapenda chifukwa mamunayu amamulonda kwambiri mkaziyo pomuganizira kuti amayenda njila zamseli.
Makawa akaonekera ku khothi kukayankha mlandu wakupha.