Malawi Broadcasting Corporation
Africa Health Local Nkhani

APEMPHA AKUFUNA KWABWINO KUTHANDIZA CHIPATALA CHA NKHOTAKOTA

Adindo pachipatala cha Nkhotakota apempha anthu akufuna kwabwino kuti athandizepo pamavuto omwe chipatalachi chikukumana nawo monga mwa zina kuchepa kwa zipinda zomwe odwala amagonamo .

Mkulu wa wachipatalachi Dr Jacob Kafulafula anena izi ku Nkhotakota atalandila thandizo la katundu wandalama zoposa K800 miliyoni lomwe bungwe la USAID kudzera muntchito ya Momentum Tikweze Umoyo lapereka m’zipatala zisanu m’dziko muno.

Adindo a chipatala cha Nkhotakota kulandira katundu

Malinga ndi mkulu wa USAID Momentum, a Marriam Mangochi, ati katunduyu athandizira ana ndi amai omwe ali ndi mavuto osiyanasiyana .

Polankhulapo Bwanankubwa wa boma la Nkhotakota, a Ben Tohno, ati thandizoli lichepetsa vuto lamayendedwe kaamba koti odwala amayenda mtunda wautali kupita mzipatala zina kaamba kosowa zipangizo zina zogwilira ntchito pachipatalachi.

Ntchito ya USAID Momentum Tikweze Umoyo mothandizana ndi AMREF Health Africa igwiridwa kwazaka zisanu m’maboma asanu m’dziko muno.

Olemba: Aisha Amidu.

Related posts

Justice ministry urges officers to harness AI

Romeo Umali

COMESA Week commences in Madagascar

McDonald Chiwayula

Kugulitsa kapena kupanga katundu osayezedwa ndi mulandu – MBS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.