Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Osamatchula anthu achi alubino maina onyazitsa- YONECO

Bungwe lolimbikitsa ufulu wa anthu a chialubino la Standing Voice lati ndi zokhumudwitsa kuti anthu ambiri akupitilira kutchula anthuwa maina onyazitsa, zomwe ati ndi kuphwanya ufulu wawo.

Mkulu wa bungweli, a Boniface Massa amayankhula izi pamene bungweli pamodzi ndi mabungwe a YONECO ndi Beyond Suncare amaphunzitsa anthu za ufulu wa anthu a chi alubino pa msika wa Govala m’boma la Zomba.

A Massa ati a Malawi akuyenera kudziwa kuti kutchula anthu achialubino maina onyazitsa zimakhumudwitsa anthuwa ndipo izi ndi nkhanza zomwe zimawabwezera m’mbuyo, zomwenso ndi kulakwila malamulo.

“Enanso akuphwanya fuku wa anthuwa ochita ukwati ndi zina zambiri. Ichi ndi chifukwa tikuyendayenda kuwadziwitsa anthu za kuyipa kosala anthu a chialubino,” atero a Massa.

Mkulu wa bungwe la YONECO, a Mac Bain Mkandawire ati kugwiritsa ntchito zisudzo ndi magule zikuthandiza kwambiri kuti anthu adzifika ndi kumva uthenga ofunikawo.

Malinga ndi mkulu oyendetsa ntchito zoti apolisi adzigwira ntchito limodzi ndi anthu m’boma la Zomba, a Naison Chibondo, mchitidwe wa nkhanza kwa anthu a chialubino ukuchepa m’bomalo.

Related posts

Mikozi ibweranso, eni ake atero

Romeo Umali

Msewu wa Nkhotakota tiumaliza komanso ukhala wapamwamba – Chakwera

MBC Online

Chakwera akutsegulira ntchito ya Millennium Challenge Corporation yokonza misewu

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.