Mwini watsamba la mchezo la Mikozi, a Bright ‘Excess’ Chiligo, watsutsa mphekesera zimene zikumveka kuti tsamba lake anthu alichita chiwembu kuti lisowe pa makina a internet.
Chiligo wati tsambali libweleranso Lachisanu chifukwa pali ntchito imene akugwira yopanga tsambali kukhala lotetezeka kwa anthu achinyengo.
“Tawona kuti pa internet pachuluka masamba a mchezo amene akubera dzina lathu la Mikozi ndipo akumayika zinthu zoyipa,” iye anatero.
Anawonjezeranso kuti zimenezi zapangitsa kuti azilandira madandaulo ochuluka kuchokera kwa anthu.