Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Msewu wa Nkhotakota tiumaliza komanso ukhala wapamwamba – Chakwera

Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, ali m’boma la Nkhotakota kumene, mwazina, akuona ntchito zachitukuko cha msewu wa M5 omwe boma la Malawi likumanga ndi thandizo lochokela ku bungwe la African Development Bank.

“Ndine wokondwa kuona kuti milatho yambiri yatha kale koma tionetsetsa kuti msewu umenewu ukhale wapamwamba,” anatero Dr Chakwera.

Pali malo angapo omwe Prezidenti Chakwera wakhala akucheza monga pa Dwangwa Trading Centre komanso pa Nkhotakota boma, pomwe pasonkhana anthu ochuluka.

Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress, a Richard Chimwendo Banda, omwe ndi nduna ya maboma ang’ono, walimbikitsa anthu m’bomali kuti alembetse maina ndicholinga choti chaka cha mawa adzakhale ndi mwayi woponya voti kuti Dr Chakwera apitirize kulamulira dziko lino ndicholinga chakuti zitukuko zipitilire m’dziko muno.

 

Wolemba: Mayeso Chikhadzula ndi Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Ntcheu Children Parliament Speaker calls for school feeding programme

MBC Online

Emmie Deebo watola chikwama

Emmanuel Chikonso

International NGOs partner local farmers for economic transformation

Doreen Sonani
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.