Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

‘Palibe chiopsezo chilichonse’

Akuluakulu a malo ogona alendo a Mount Soche munzinda wa Blantyre ati akwanitsa kuzimitsa moto umene unabuka pamalowo.

Malinga ndi mmodzi mwa akuluakuluwo, motowo unabuka ku malo komwe amatayako zinyalala.

Iwo ati motowo sunakhudze malo eni-eni ogona alendo.

Pakadali pano, akuluakuluwo apempha alendo komanso ogwira ntchito amene anathawa pamalopo kuti abwelere, ponena kuti palibe chiwopsezo chilichonse.

 

Related posts

‘Kalembetseni chiphaso cha unzika kuti mudzavote’

Romeo Umali

UNICEF ipitiliza kuthandiza Mtukula Pakhomo

Alinafe Mlamba

Amagulitsa mwana wake wazaka zitatu

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.